Malaŵi ndziko lokongola, La chonde ndi ufulu, Nyanja ndi mphepo ya m’mapiri, Ndithudi tadala. Zigwa, mapiri, nthaka, dzinthu, N’mphatso zaulere. Nkhalango, madambo abwino. Ngwokoma Malaŵi.
O Ufulu tigwirizane, Kukweza Malaŵi. Ndi chikondi, khama, kumvera, Timutumikire. Pa nkhondo nkana pa mtendere, Cholinga n’chimodzi. Mai, bambo, tidzipereke, Pokweza Malaŵi.